baibulo - Akamaihd.net
Transcription
Na. 4, 2016 34567 BAIBULO BUKU LOMWE LINAPULUMUKA M’ZAMBIRI 34567 Vol. 137, Na. 10 CHICHEWA Makope 58,987,000 a Magaziniyi Asindikizidwa M’ZINENERO 267 KODI MUKUGANIZA BWANJI? MAGAZINI ya Nsanja ya Olonda imalemekeza Yehova Mulungu, yemwe ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse. Imalimbikitsa anthu ndi uthenga wabwino wakuti Ufumu wa Mulungu posachedwapa uchotsa zoipa zonse n’kusintha dziko lapansili kukhala paradaiso. Imalimbikitsa anthu kukhulupirira Yesu Khristu yemwe anatifera kuti tipeze moyo wosatha ndipo panopo akulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Magaziniyi yakhala ikufalitsidwa kuyambira mu 1879 ndipo si yandale. Mfundo zake zimachokera m’Baibulo. Magaziniyi sitigulitsa. Timaipereka ngati njira imodzi yophunzitsira anthu Baibulo padziko lonse ndipo ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Ngati mukufuna kupereka ndalama zothandizira pa ntchito yolalikira pitani pa www.jw.org. Malemba onse m’magaziniyi akuchokera mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika, kupatulapo ngati tasonyeza Baibulo lina. Kodi mukufuna kudziwa zambiri kapena kuphunzira Baibulo kwaulere? Pitani pa www.jw.org/ny kapena tumizani pempho lanu pogwiritsa ntchito adiresi yoyenera pa maadiresi omwe ali m’munsiwa. Na. 4, 2016 Ngati Baibulo si buku lochokera kwa Mulungu, kodi likanapulumuka m’zinthu zonsezi? Baibulo limanena kuti: “Udzu wobiriwirawo wauma. Maluwawo afota. Koma mawu a Mulungu wathu adzakhala mpaka kalekale.”—Yesaya 40:8. Nkhanizi zikufotokoza mfundo zochititsa chidwi zokhudza mmene Baibulo linapulumukira m’zinthu zosiyanasiyana. Baibulo—Buku Lomwe Linapulumuka M’zambiri Kodi Kudziwa Mmene Baibulo Linapulumukira N’kothandiza? 3 Baibulo Linasungidwa Bwino Kuti Lisawole 4 Baibulo Linapulumuka Ngakhale Kuti Ena Sankalifuna 5 Baibulo Linapulumuka Ngakhale Kuti Ena Ankafuna Kusintha Uthenga Wake 6 N’chifukwa Chiyani Baibulo Linapulumuka? 8 M’MAGAZINIYI MULINSO NKHANI IZI Kodi Mukudziwa? 9 Kodi Zachiwawa Zidzatha Padzikoli? 10 Baibulo Limasintha Anthu Ndinasintha Khalidwe Langa Movutikira Kwambiri 12 Kodi Mungayerekezere Zimene Mumakhulupirira ndi Zimene Baibulo Limaphunzitsa? 14 Kodi Baibulo Limanena Zotani? 16 The Watchtower (ISSN 0043-1087) Issue 10 July 2016 is published monthly with an additional issue published in January, March, May, July, September, and November by Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.; L. Weaver, Jr., President; G. F. Simonis, Secretary-Treasurer; 1000 Red Mills Road, Wallkill, NY 12589-3299, and printed by Watch Tower Bible and Tract Society of South Africa NPC, 1 Robert Broom Drive East, Rangeview, Krugersdorp, 1739. 5 2016 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Printed in South Africa. s MUNGAWERENGENSO NKHANI ZINA PAWEBUSAITI YATHU MUNGAPEZE YANKHO LA M’BAIBULO LA FUNSO ILI Kodi Baibulo Ndi Lochokera kwa Mulungu? r (Pitani pamene palembedwa kuti, ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA ˛ KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO) NKHANI YA PACHIKUTO Kodi Kudziwa Mmene Baibulo Linapulumukira N’kothandiza? Palibe buku lina lililonse la chipembedzo lomwe lingapose Baibulo, chifukwa lakhala likuthandiza anthu kuti azikhulupirira zinthu zolondola. Komanso ndi buku lokhalo limene anthu alifufuza kwambiri ndiponso kulipezera zifukwa. Akatswiri ena amakaikira ngati uthenga wa m’Mabaibulo a masiku ano ulidi wofanana ndi womwe unali m’mipukutu yoyambirira. Mwachitsanzo, pulofesa wina wamaphunziro azachipembedzo ananena kuti: “Sitinganene motsimikiza kuti tinakoperadi uthenga wa m’Baibulo molondola chifukwa Mabaibulo ambiri ali ndi zinthu zolakwika zokhazokha. Komanso analembedwa patadutsa zaka zambiri kuchokera pamene mipukutu yoyambirira inalembedwa, choncho uthenga wake ndi wosiyana kwambiri ndi womwe unali m’mipukutuyi.” Anthu enanso amakhulupirira kuti uthenga wa m’Baibulo unasinthidwa chifukwa ndi zomwe anaphunzitsidwa kuzipembedzo zawo. Mwachitsanzo Faizal, anauzidwa ndi anthu a m’banja lake omwe si Akhristu, kuti Baibulo ndi buku lopatulika koma linasinthidwa. Iye anati: “Chifukwa cha zimenezi, anthu akamandifotokozera zokhudza Baibulo ndinkakayikira kwambiri uthenga wake. Ndinkaona kuti si lolondola chifukwa linasinthidwa.” Kodi kudziwa ngati Baibulo linasinthidwa kapena ayi kuli ndi phindu lililonse? Kuti mupeze yankho la funsoli, taganizirani mafunso awa: Kodi zikanakhala kuti zinthu zabwino zimene Baibulo limalonjeza sizinalembedwe m’mipukutu yoyambirira, mukanazikhulupirira? (Aroma 15:4) Zikanakhala kuti mfundo zonse za m’Mabaibulo a masiku ano ndi zolakwika, kodi mukanazigwiritsa ntchito posankha zochita pa nkhani zokhudza ntchito, banja kapena kupembedza Mulungu? Ngakhale kuti mipukutu yoyambirira ya Baibulo sikupezeka, pali zolemba zina zakale komanso mipukutu ina yambiri ya Baibulo imene imatithandiza. Kodi zinatheka bwanji kuti mipukutuyi izipezekabe masiku ano? Funsoli ndi lofunika chifukwa anthu ena ankafuna kuithetseratu, kusintha uthenga wake komanso ikanatha kuwola. Kodi kupezeka kwa mipukutuyi kungakuthandizeni bwanji kukhulupirira kuti uthenga wa m’Baibulo ndi wolondola? Kuti mudziwe mayankho a mafunsowa, werengani nkhani zokhudza mmene Baibulo linapulumukira ku zinthu zonsezi. Na. 4, 2016 3 Baibulo Linasungidwa Bwino Kuti Lisawole VUTO LIMENE LINALIPO: Anthu omwe ankalemba komanso kukopera mipukutu ya Baibulo ankagwiritsa ntchito gumbwa komanso zikopa. (2 Timoteyo 4:13) Komatu zimenezi zikanachititsa kuti mipukutuyi iwonongeke mosavuta. N’chifukwa chiyani tikutero? Gumbwa amang’ambika, kusuluka komanso kutha mosavuta. Richard Parkinson ndi Stephen Quirke, anaphunzira zinthu zosiyanasiyana za ku Egypt ndipo anati: “Gumbwa akhoza kuwola n’kutsala ulusi kapenanso fumbi lokhalokha. Mpukutu ukakhala nthawi yaitali umachita nkhungu kapenanso kuwola chifukwa cha chinyezi ndipo akaukwirira umadyedwa ndi chiswe.” Komanso mipukutu ina ya gumbwa itapezeka, sinasungidwe bwino ndipo inawonongeka chifukwa cha chinyezi komanso kuwala. Mipukutu ya chikopa imakhala yolimba kusiyana ndi ya gumbwa. Koma nayonso imawonongeka ikasungidwa pamalo otentha, achinyezi kapenanso owala kwambiri.1 Mipukutuyi imadyedwanso ndi tizilombo. Buku lina linanena kuti: “Kawirikawiri mipukutu yakale siikhalitsa.” (Everyday Writing in the Graeco-Roman East) Choncho zikanakhala kuti mipukutu ya Baibulo inawola, uthenga wake ukanatheranso pomwepo. 1 Mwachitsanzo, chikalata cholengeza kuti dziko la United States ndi lodziimira palokha (U.S. Declaration of Independence), chinalembedwa pachikopa. Panopa padutsa zaka zosapitirira 250 kuchokera nthawi yomwe chikalatachi chinalembedwa, koma zilembo zake zimavuta kuwerenga chifukwa zinafufutika. ZOTSATIRA ZAKE: Mipukutu yambiri ya Baibulo idakalipo ndipo yakhalapo kwa zaka zoposa 2,000. Kunena zoona palibenso mipukutu ya mabuku ena akale yomwe yakhalapo kwa nthawi yaitali chonchi. ZIMENE ZINATHANDIZA KUTI BAIBULO LISUNGIKE: Lamulo lachiyuda linkalimbikitsa mfumu iliyonse kuti izikopera “buku lakelake la chilamulo” lomwe ndi mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo. (Deuteronomo 17:18) Komanso pofika chakumapeto kwa nthawi ya atumwi n’kuti akatswiri okopera malemba atakopera mipukutu yambiri. Zimenezi zinathandiza kuti malemba azipezeka m’masunagoge a ku Isiraeli ngakhalenso kumadera akutali monga ku Makedoniya. (Luka 4:16, 17; Machitidwe 17:11) Komano zinatheka bwanji kuti mipukutuyi isungidwe mpaka pano? Katswiri wina wa Chipangano Chatsopano dzina lake Philip W. Comfort ananena kuti: “Ayuda ankakonda kusunga mipukutu m’mitsuko n’cholinga choti isawonongeke.” Ndipo zikuoneka kuti Akhristu nawonso ankachita zomwezo chifukwa mipukutu ina yoyambirira ya Baibulo inapezeka m’mitsuko, m’zipinda zamdima ndi m’mapanga a m’madera otentha kwambiri. Photograph taken by courtesy of the British Museum Shrine of the Book, Photo 5 The Israel Museum, Jerusalem Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa inasungidwa kwa zaka zambiri m’mitsuko yomwe inaikidwa m’mapanga, m’madera ouma Baibulo Linapulumuka Ngakhale Kuti Ena Sankalifuna VUTO LIMENE LINALIPO: Atsogoleri ambiri andale komanso azipembedzo sankafuna kuti anthu adziwe uthenga wa m’Baibulo. Choncho iwo ankagwiritsa ntchito udindo wawo poletsa anthu kumasulira, kusindikiza ngakhalenso kukhala ndi Baibulo. Tiyeni tione zitsanzo ziwiri: ˙ Cha m’ma 167 B.C.E.: Mfumu Antiyokasi Epifanasi yemwe ankafuna kukakamiza Ayuda kuti azitsatira chipembedzo chachigiriki, analamula kuti Malemba onse Achiheberi awonongedwe. Wolemba mbiri wina dzina lake Heinrich Graetz, ananena kuti nduna za mfumuyi “zikapeza mipukutu ya Chilamulo, zinkaing’amba ndiponso kuitentha nthawi yomweyo. Komanso zinkapha aliyense amene wapezeka akuwerenga Baibulo pofuna kulimbikitsidwa ndiponso kutonthozedwa.” ˙ Zaka za m’ma 500 mpaka 1500: Atsogoleri ena achikatolika ankakhumudwa chifukwa choti anthu a m’chipembedzochi ankalimbikitsa ena kutsatira mfundo za m’Baibulo m’malo mwa zikhulupiriro zachikatolika. Iwo ankafuna kuti anthu aziwerenga buku la Masalimo la m’Chilatini basi. Ndipo anthu wamba omwe anali ndi mabuku ena a m’Baibulo, ankawanena kuti ndi ampatuko. Pamsonkhano wina wa tchalitchichi anasankha anthu oti “azifufuza mwakhama anthu ampatuko . . . m’nyumba ndiponso m’zipinda zonse zapansi, zomwe ankazikayikira kuti akusungirako mabuku a m’Baibulo. . . . Ndipo nyumba iliyonse yomwe apezako wampatuko, aziigwetsa.” Anthuwa akanakwanitsadi kuwononga Baibulo, ndiye kuti uthenga wake ukanatheranso pomwepo. lira ndi kukopera Baibulo pamanja. Zikuoneka kuti pofika cha m’ma 1400, mabuku ena a m’Baibulo ankapezeka m’zinenero pafupifupi 33, ngakhale kuti pa nthawiyi kunalibe makina osindikizira mabuku. Patapita nthawi, anthu anayamba kumasulira komanso kusindikiza Mabaibulo m’zinenero zinanso zambiri. ZOTSATIRA ZAKE: M’nkhaniyi taona kuti atsogoleri ena andale komanso azipembedzo ankafuna kuwononga Baibulo, koma sizinatheke. Baibulo lamasuliridwa komanso kufalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse. Lathandizanso mayiko ambiri pa nkhani zokhudza malamulo ndi zinenero. Komanso lathandiza anthu ambiri kusiya makhalidwe oipa. ZIMENE ZINATHANDIZA KUTI BAIBULO LISUNGIKE: Ngakhale kuti Mfumu Antiyokasi inkafuna kuti Baibulo lisapezekenso ku Isiraeli, Ayuda ambiri anali atasamukira m’mayiko osiyanasiyana. Ndipotu akatswiri amanena kuti pomwe inkafika nthawi ya Yesu, n’kuti Ayuda oposa 60 pa 100 alionse akukhala m’madera a kunja kwa dziko la Isiraeli. Ayudawa ankasunga mipukutu ya Malemba m’masunagoge awo ndipo ndi yomwenso anthu ena kuphatikizapo Akhristu, ankaigwiritsa ntchito.—Machitidwe 15:21. M’zaka za m’ma 500 mpaka 1500, anthu ena analimba mtima n’kulolera kuzunzidwa ndipo anapitiriza kumasu- Baibulo lachingelezi lomasuliridwa ndi William Tyndale, linapulumuka ngakhale kuti pa nthawiyi Mabaibulo ena analetsedwa komanso kuwotchedwa. William anaphedwa mu 1536. Na. 4, 2016 5 Baibulo Linapulumuka Ngakhale Kuti Ena Ankafuna Kusintha Uthenga Wake VUTO LIMENE LINALIPO: M’nkhani zapitazi taona kuti Baibulo linasungidwa bwino ngakhale kuti likanawola komanso panali anthu omwe sankalifuna. Komabe pali anthu ena omwe ankafuna kusintha uthenga wake. Nthawi zina m’malo mophunzitsa mfundo za m’Baibulo, iwo ankasintha uthenga wake kuti ugwirizane ndi ziphunzitso zawo. Taonani zitsanzo izi: ˙ Malo olambirira: M’zaka za pakati pa 300 ndi 100 B.C.E., Asamariya ena omwe anamasulira Pentatuke Wachisamariya (mabuku 5 oyambirira a m’Baibulo), anawonjezera mawu patsogolo pa Ekisodo 20:17 akuti: “Ku Gerizimu mudzamangako kachisi.” Iwo ankafuna kuti Malemba azigwirizana ndi zimene ankafuna zoti adzamange kachisi m’phiri la “Aargaareezem,” kapena kuti Gerizimu. ˙ Chiphunzitso cha utatu: Pasanathe zaka 300 kuchokera pamene Baibulo linamalizidwa kulembedwa, wolemba mabuku wina yemwe ankakhulupirira utatu anawonjezera mawu pa 1 Yohane 5:7, akuti, “Kumwamba kuli Atate, Mawu, komanso Mzukwa Woyera: onsewa ndi mmodzi.” Katswiri wina wa Baibulo dzina lake Bruce Metzger, ananena kuti, “Kungoyambira mu 500 C.E., mawu amenewa ankapezeka kwambiri m’mipukutu yachilatini chakale komanso m’Baibulo lachilatini lotchedwa Vulgate.” ˙ Dzina la Mulungu: Omasulira Baibulo ambiri anaganiza zochotsa dzina la Mulungu m’Baibulo chifukwa cha zomwe Ayuda ankakhulupirira zoti akatchula dzina la Mulungu akhoza kuona malodza. Ndiyeno anayamba kumangogwiritsa ntchito maina audindo monga “Mulungu” kapena “Ambuye.” Komatu nthawi zina m’Baibulo mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za anthu, mafano ngakhalenso Mdyerekezi.—Yohane 10: 34, 35; 1 Akorinto 8:5, 6; 2 Akorinto 4:4.1 Mpukutu wa Baibulo wopangidwa ndi gumbwa wa m’ma 200 C.E., womwe unasungidwa mu Laibulale ya Chester Beatty P46. 5The Trustees of the Chester Beatty Library, Dublin ZIMENE ZINATHANDIZA KUTI BAIBULO LISUNGIKE: Choyamba, ngakhale kuti anthu ena ankafuna kusintha uthenga wa m’Baibulo, panali ena ambiri amene ankakopera Malemba mwaluso komanso mosamala. Mwachitsanzo, m’zaka za m’ma 500 ndi 900 C.E., Amaso1 Kuti mudziwe zambiri, Onani Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu tsamba 1-13. Kabukuka kakupezekanso pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny. 6 NSANJA YA OLONDA “Tinganenedi motsimikiza kuti palibenso buku lina lakale lomwe linamasuliridwa ndiponso kukopedwa molondola kuposa Baibulo” rete anakopera Malemba Achiheberi n’kupanga buku lomwe limadziwika kuti Zolemba za Amasorete. Iwo akamakopera, ankawerenga liwu lililonse pofuna kutsimikizira kuti sanawonjezeremo mfundo zolakwika. Ngati akukayikira kuti mumpukutu womwe akugwiritsa ntchitowo muli mfundo zolakwika, ankalemba mfundozo m’mphepete mwa mpukutuwo. Amasorete sankafuna kusintha uthenga wa m’Baibulo ngakhale pang’ono. Pulofesa wina dzina lake Moshe Goshen-Gottstein analemba kuti: “Iwo ankadziwa kuti kusintha uthenga wa m’Baibulo mwadala unali mlandu waukulu.” Chachiwiri, masiku ano pali mipukutu yambiri yomwe inapezeka. Choncho akatswiri a Baibulo savutika kudziwa ngati pali mfundo zina zosiyana ndi za m’mipukutu yoyambirira. Mwachitsanzo, kwa zaka zambiri atsogoleri azipembedzo ankaphunzitsa kuti Mabaibulo awo Achilatini anali odalirika kwambiri. Koma chodabwitsa n’choti pa 1 Yohane 5:7 anaphatikizapo mawu olakwika aja omwe tawatchula kumayambiriro kwa nkhaniyi. Ndipotu mawuwa anawaphatikizanso m’Baibulo la King James. Komano mipukutu ina itapezeka, m’pamene anazindikira kuti m’mipukutu yaka- Amasorete ankakopera Malemba mosamala kwambiri le munalibe mawuwa. Bruce Metzger analemba kuti: “M’mipukutu yakale (monga ya Chiameniya, Chiitiopiya, Chikoputiki, Chiarabu ndi Chisilaviki), mulibe mawu omwe anawawonjezera [pa 1 Yohane 5:7], kupatulapo m’mpukutu wa Chilatini tautchula uja. N’chifukwa chake m’mabaibulo ena okonzedwanso monga la King James anachotsamo mawu olakwikawa. Kodi mipukutu yakale imatsimikiziradi kuti uthenga wa m’Baibulo sunasinthe? Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa itapezeka mu 1947, akatswiri anali ndi mwayi woyerekezera Zolemba za Amasorete ndi zimene zinali m’mipukutuyi, yomwe inalembedwa zaka zoposa 1,000 m’mbuyomo. Munthu wina yemwe anakonza nawo mipukutu ya ku Nyanja Yakufa ananena kuti mpukutu umodzi wokha “unapereka umboni wosatsutsika wosonyeza kuti ntchito yokopera Malemba yomwe okopera Achiyuda anagwira m’zaka zopitirira 1,000, inachitika mwaluso ndiponso mosamala kwambiri.” Mumzinda wa Dublin, ku Ireland muli Laibulale yotchedwa Chester Beatty komwe anasungako pafupifupi mipukutu yonse ya Malemba Achigiriki Achikhristu yopangidwa ndi gumbwa. Ina mwa mipukutuyi ndi ya m’zaka za m’ma 100 C.E., zomwe zikusonyeza kuti yangokhalapo kwa zaka 100 zokha, kuchokera pamene Baibulo linamalizidwa kulembedwa. Buku lina linanenanso kuti, “mipukutu ya gumbwa imatsimikizira kuti uthenga wa m’Baibulo unalembedwa mwatsatanetsatane komanso kuti uthengawu sunasinthidwe paliponse.” —The Anchor Bible Dictionary. ZOTSATIRA ZAKE: Mipukutu yambiri yakale yomwe inapezeka yathandiza kuti uthenga wa m’Baibulo ukhale wolondola. Katswiri wina dzina lake Frederic Kenyon analemba zokhudza Malemba Achigiriki Achikhristu kuti: “Palibenso buku lina lakale lomwe lili ndi umboni wotsimikizira kuti ndi lolondola kuposa Baibulo, ndipo palibe katswiri aliyense woganiza bwino yemwe angatsutse zoti uthenga womwe tili nawowu ndi wodalirika.” Ponena za Malemba Achiheberi, katswiri wina dzina lake William Henry Green, ananena kuti: “Tinganenedi motsimikiza kuti palibenso buku lina lakale lomwe linamasuliridwa ndi kukopedwa molondola kuposa Baibulo.” Na. 4, 2016 7 N’chifukwa Chiyani Baibulo Linapulumuka? Masiku ano mukhoza kupeza ndiponso kuwerenga Baibulo mosavuta. Ndipo ngati mwasankha Baibulo lomwe linamasuliridwa molondola, m’posavuta kutsimikizira kuti uthenga wake ndi wochokeradi m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo.1 M’nkhani 1 Onani nkhani yakuti, “Kodi Mungadziwe Bwanji Baibulo Lomasuliridwa Bwino?” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2008. zapitazi taona kuti Baibulo linapulumuka ngakhale kuti likanatha kuwola, anthu ena ankalitsutsa, komanso ankafuna kusintha uthenga wake. Koma n’chifukwa chiyani linapulumuka modabwitsa chonchi? Anthu ambiri amene akuphunzira Baibulo amavomereza zomwe mtumwi Paulo analemba kuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Anthuwa amakhulupirira kuti Baibulo linapulumuka chifukwa chakuti ndi Mawu a Mulungu komanso Iye analiteteza. Faizal yemwe watchulidwa m’nkhani yoyambirira, anaganiza zoyamba kuphunzira Baibulo pofuna kutsimikizira zimenezi. Iye anadabwa ataona kuti zinthu zambiri zimene anthu amaphunzitsa m’matchalitchi awo sizichokera m’Baibulo. Faizal anachita chidwi kwambiri ataphunzira cholinga cha Mulungu chokhudza dziko lapansi kuchokera m’Baibulo. Iye ananena kuti: “Panopa sindikukayika ngakhale pang’ono kuti Baibulo lomwe ndili nalo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Komanso ngati Mulungu yemwe ndi Wamphamvuyonse anakwanitsa kulenga chilengedwechi, kodi angalephere kutipatsa buku ndi kuliteteza kuti tiziliwerenga? Munthu yemwe angatsutse zimenezi ndiye kuti akuderera mphamvu za Mulungu, yemwe ndi Wamphamvuyonse, nanga ine ndani kuti ndichite zimenezi?”—Yesaya 40:8. ˇ w “Panopa sindikukayika ngakhale pang’ono kuti Baibulo lomwe ndili nalo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu” 8 NSANJA YA OLONDA Nkhanizi zafotokoza zomwe zinathandiza kuti Baibulo lisawonongedwe. Koma n’chiyani chingakutsimikizireni kuti Baibulo ndi “mawu a Mulungu” osati buku la nthano zongolembedwa ndi anthu? (1 Atesalonika 2:13) Tikukulimbikitsani kuti muonere vidiyo ya pa jw.org/ny yakuti, Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona? (Pitani pamene palembedwa kuti, MABUKU MAVIDIYO) KODI MUKUDZIWA? Kodi Yesu ankasiyana bwanji ndi Arabi pochita zinthu ndi anthu akhate? Kale Ayuda ankachita mantha kwambiri ndi matenda a khate omwe amatchulidwa m’Baibulo. Matendawa anali oopsa chifukwa ankagwira mitsempha yotumiza uthenga ku ubongo ndipo zinkachititsa kuti munthu alumale. Pa nthawiyi kunalibe mankhwala a khate. Ndipo odwala matendawa ankawaika kwaokha komanso ankayenera kuchenjeza ena za matenda awowo.—Levitiko 13:45, 46. Atsogoleri achiyuda anakhazikitsa malamulo okhwima komanso osagwirizana ndi zomwe Mawu a Mulungu ankanena zokhudza anthu akhate. Zimenezi zinkachititsa kuti anthuwa azivutika kwambiri. Mwachitsanzo, arabi anakhazikitsa malamulo akuti munthu aliyense akaona wakhate azitalikirana naye mamita awiri. Komanso ankanena kuti ngati kukuwomba mphepo, azitalikirana naye mamita 45. Buku la malamulo ndi miyambo ya Ayuda (Talmud), linati lamulo la m’Baibulo loti akhate “azikhala kunja kwa msasa,” linkatanthauza kuti sayenera kukhala mumzinda uliwonse wampanda. Arabi akaona wakhate ali mumzinda, ankamugenda n’kumuuza kuti: “Pita kumalo ako, usapatsire anthu ena matenda akowo!” Komatu Yesu ankachita zinthu zosiyana kwambiri ndi atsogoleriwa. Iye sankathamangitsa akhate, koma ankafunitsitsa kuwakhudza ndiponso kuwachiritsa.—Mateyu 8:3. ˇ Kodi atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankalola kuti mwamuna asiye mkazi wake pa zifukwa ziti? KALATA YOTHETSERA UKWATI YA ZAKA ZA M’MA 71 KAPENA 72 C.E. Courtesy Israel Antiquities Authority Kale atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankasiyana maganizo pa nkhani ya zifukwa zomwe mwamuna angathetsere ukwati. Mwachitsanzo, nthawi ina Afarisi anafunsa Yesu kuti: “Kodi n’kololeka kuti mwamuna asiye mkazi wake pa chifukwa chilichonse?”—Mateyu 19:3. Chilamulo cha Mose chinkalola mwamuna kusiya mkazi wake ngati “wam’peza ndi vuto linalake.” (Deuteronomo 24:1) M’nthawi ya Yesu, kunali sukulu ziwiri zomwe ankaphunzitsirako arabi kapena kuti aphunzitsi achiyuda. Kusukuluzi ankaphunzitsa mfundo zosiyana zokhudza lamuloli. Mwachitsanzo, kusukulu ya Shammai ankaphunzitsa mfundo zokhwima ndipo ankati ukwati ukhoza kutha pokhapokha ngati wina wachita chigololo. Pomwe kusukulu ya Hillel ankaphunzitsa kuti mwamuna akhoza kusiya mkazi wake chifukwa cha vuto lina lililonse la m’banja ngakhale laling’ono. Mwachitsanzo, ankaphunzitsa kuti mwamuna akhoza kuthetsa ukwati ngati mkazi wake sanaphike bwino chakudya kapenanso akaona mkazi wina wokongola. Kodi Yesu anayankha bwanji funso la Afarisi? Iye ananena mosabisa mawu kuti: “Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.”—Mateyu 19:6, 9. ˇ Na. 4, 2016 9 KODI ZACHIWAWA ZIDZATHA PADZIKOLI? Kodi inuyo kapena munthu wina wa m’banja lanu anachitiridwapo zinthu zachiwawa? Kodi mumachita mantha kuti tsiku lina zidzakuchitikirani? Anthu ena amanena kuti zachiwawa “zikuchuluka padziko lonse ndipo zikuchititsa kuti anthu azikumana ndi mavuto azaumoyo.” Taonani zitsanzo izi: NKHANZA ZA M’BANJA KOMANSO ZOKHUDZA KUGONANA: Lipoti lina la bungwe la United Nations linanena kuti: “Mayi mmodzi pa atatu alionse anamenyedwapo ndi mwamuna wake kapenanso kuchitiridwa nkhanza zokhudza kugonana ndi munthu womudziwa. Komanso mayi mmodzi pa amayi 5 alionse akhoza kugwiriridwa.” UCHIFWAMBA NDI UMBANDA: Malipoti amasonyeza kuti ku United States kokha kuli magulu a zauchifwamba oposa 30,000. Ndipo ku Latin America pafupifupi munthu mmodzi pa atatu alionse anachitiridwapo zauchifwamba. KUPHA ANTHU MWACHISAWAWA: Kafukufuku amasonyeza kuti m’chaka cha 2012 chokha, anthu pafupifupi 500,000 anaphedwa ndi zigawenga padziko lonse. Chiwerengerochi ndi chachikulu poyerekezera ndi anthu omwe anaphedwa pa nkhondo m’chakachi. Mayiko a kum’mwera kwa Africa komanso ku Central America ndi omwe anali ndi chiwerengero chokwera kwambiri cha anthu ophedwa. Mwachitsanzo, ku Latin America kunaphedwa anthu oposa 100,000 m’chaka cha 2013, ndipo ku Brazil kunaphedwa anthu oposa 50,000. Kodi pamenepa tinganene kuti zachiwawa zidzatha padzikoli? KODI N’ZOTHEKA KUTHETSA ZACHIWAWA? N’chifukwa chiyani zachiwawa zikuchitika padziko lonse? Pali zifukwa zambiri monga izi: Kuponderezana pakati pa anthu olemera ndi osauka, uchidakwa, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kuona moyo wa anthu ena ngati wosafunika komanso kukulira m’banja kapena m’dera lomwe anthu amakonda zachiwawa. Anthu enanso amachita zachiwawa chifukwa chakuti anthu ambiri ochita khalidweli sapatsidwa chilango chokhwima. Komabe mayiko ena akuyesetsa kuchepetsa zachi˜ Paulo, ku wawa. Mwachitsanzo, mumzinda wa Sao Brazil, chiwerengero cha anthu ophedwa mwachisawawa chatsika kwambiri m’zaka 10 zapitazi. Ngakhale zili choncho, zauchifwamba zimachitikabe mobwerezabwereza moti anthu 10 pa 100,000 amaphedwa. 10 NSANJA YA OLONDA Ndiyeno funso n’kumati, n’chiyani chingathandize kuti zachiwawa zitheretu padziko lonse? Kuti zachiwawa zitheretu, anthu afunika kusintha mmene amaonera zinthu komanso khalidwe lawo. Mwachitsanzo, ayenera kusiya kunyada, umbombo ndi kudzikonda, n’kuyamba kukhala achikondi, aulemu ndiponso oganizira ena. Kodi n’chiyani chingathandize munthu kuti asiye makhalidwe oipa? Taonani zimene Baibulo limaphunzitsa: ˇ “Chifukwa kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 Yohane 5:3. ˇ “Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.”1—Miyambo 8:13. 1 Dzina la Mulungu ndi Yehova ndipo limapezeka m’Baibulo. Anthu achiwawa angasinthe khalidwe lawo ngati atamakonda Mulungu komanso kupewa zinthu zomwe zingamukhumudwitse. Ndipotu zimenezi n’zotheka. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Alex,1 amene anakhala m’ndende ina ya ku Brazil kwa zaka 19, chifukwa cha milandu yosiyanasiyana yomenya ndi kuvulaza anthu. Iye anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova ndipo anabatizidwa mu 2000. Kodi anasinthadi khalidwe lakeli? Alex anasinthiratu ndipo anati: “Panopa ndimakonda kwambiri Mulungu chifukwa ndimadziwa kuti anandikhululukira. Komatu ndinasiya makhalidwewa chifukwa chokonda Mulungu komanso kusafuna kumukhumudwitsa.” ´ Cesar wa ku Brazil ankathyola nyumba za anthu komanso kuba moopseza ndi mfuti. Iye anachita zimenezi kwa zaka 15. Ndiye n’chiyani chinamuthandiza kuti asinthe? Pa nthawi imene anali kundende, anakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo anayamba ku´ phunzira Baibulo. Cesar anafotokoza kuti: “Nditangoyamba kuphunzira, ndinazindikira cholinga cha moyo ndiponso ndinayamba kukonda Mulungu komanso kumuopa. Zimenezi zinandithandiza kuti ndisiyiretu kuchita zinthu zoipa zomwe amadana nazo. Sindinkafunanso kuchita chilichonse chosonyeza kuti sindikuyamikira chifundo chake. Choncho ndinasintha khalidwe langa.” ´ Zimene zinachitikira Alex ndi Cesar, zikusonyeza kuti Baibulo lili ndi mphamvu zothandiza anthu kusintha zochita komanso maganizo oipa. (Aefeso 4:23) Alex ananenanso kuti: “Zimene ndinaphunzira m’Baibulo zinali ngati madzi oyera bwino omwe ankayeretsa makhalidwe anga pang’onopang’ono. Ndinali ndisanaganizepo kuti ndingadzasinthe chonchi.” Uwu ndi umboni wakuti tikamawerenga uthenga wa m’Baibulo womwe ndi woyera, tingathe kuchotsa maganizo alionse oipa mumtima mwathu. Mawu a Mulungu alidi ndi mphamvu yoyeretsa maganizo a anthu. (Aefeso 5:26) Monga mmene taonera, anthu omwe kale anali ndi makhalidwe oipa akhoza kusintha n’kukhala achifundo komanso amtendere. (Aroma 12:18) Ndipo akamatsatira mfundo za m’Baibulo, amakhalanso ndi mtendere wamumtima.—Yesaya 48:18. A Mboni za Yehova opitirira 8 miliyoni omwe akupezeka m’mayiko oposa 240, akudziwa bwino chimene chingathandize kuti zachiwawa zitheretu. Ngakhale kuti ndi ochokera m’mitundu yosiyanasiyana, onse 1 Mayina asinthidwa. Phunzirani zimene mungachite kuti mudzakhale m’dziko lopanda chiwawa amakonda Mulungu komanso kumuopa. Amakondananso kwambiri ndipo amakhala mwamtendere ngati banja limodzi. (1 Petulo 4:8) Umenewutu ndi umboni wakuti n’zotheka kuthetsa zachiwawa padzikoli. ZINTHU ZACHIWAWA ZITHA POSACHEDWAPA Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa Mulungu athetsa zachiwawa zonse padzikoli. Ndipo limatitsimikizira kuti anthu onse okonda zachiwawa adzaphedwa “m’tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu.” (2 Petulo 3:5-7) Pa nthawiyi sikudzakhalanso anthu ozunza ena. Koma kodi tingatsimikize bwanji kuti Mulungu ndi wofunitsitsa kuthetseratu zachiwawa? Baibulo limanena kuti “Mulungu amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.” (Salimo 11:5) Mlengi wathu amakonda mtendere ndi chilungamo. (Salimo 33:5; 37:28) N’chifukwa chake sadzalola kuti anthu ochita zachiwawa akhalepo mpaka kalekale. Dziko latsopano komanso lamtendere layandikira. (Salimo 37:11; 72:14) Choncho tikukulimbikitsani kuti muyambe kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova kuti mudziwe zimene mungachite kuti mudzakhale nawo m’dziko limeneli. ˇ w Onerani vidiyo yakuti, “Zinthu Zinayamba Kuyenda Bwino” pawebusaiti ya www.jw.org/ny, kuti muone zimene bambo wina ankachita asanaphunzire Baibulo. (Pitani pamene palembedwa kuti MABUKU MAVIDIYO) BAIBULO LIMASINTHA ANTHU Ndinasintha khalidwe langa movutikira kwambiri YOFOTOKOZEDWA NDI JOSEF MUTKE CHAKA CHOBADWA 1953 DZIKO AUSTRALIA POYAMBA NDINKAKONDA KUONERA ZOLAULA 12 NSANJA YA OLONDA KALE LANGA: Bambo anga anachoka ku Germany kupita ku Australia mu 1949, kukafufuza ntchito m’makampani a migodi ndi magetsi. Iwo anakakhala m’mudzi wina wotchedwa Victoria, ndipo n’komwe anakwatirana ndi mayi anga. Ineyo ndinabadwa mu 1953. Patangodutsa zaka zochepa, mayi anga anayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Choncho ndinayamba kumva mfundo za m’Baibulo ndili wamng’ono. Koma bambo anga ankadana ndi chipembedzo chilichonse, ndipo anayamba kutichitira nkhanza kwambiri. Mayi anga ankakhala mwamantha moti ankaphunzira Baibulo mobisa. Komabe anayamba kukonda zomwe ankaphunzirazo. Bambo akachoka, amayi ankapeza mpata wofotokozera ineyo ndi mchemwali wanga zimene aphunzira m’Baibulo. Ankatiuza kuti dzikoli lidzakhala paradaiso komanso kuti tingakhale osangalala ngati titamatsatira mfundo za m’Baibulo.—Salimo 37:10, 29; Yesaya 48:17. Ndili ndi zaka 18, ndinachoka pakhomo chifukwa cha nkhanza za bambo anga. Ngakhale kuti ndinkakhulupirira zonse zomwe amayi anandiphunzitsa, sindinkazigwiritsa ntchito. Kenako ndinayamba ntchito ya zamagetsi m’migodi ya malasha. Ndinakwatira ndili ndi zaka 20, ndipo patadutsa zaka zitatu, tinabereka mwana wamkazi. Kenako ndinaganiza zoyambiranso kuphunzira Baibulo chifukwa ndinkadziwa ndithu kuti mfundo zake zikhoza kuthandiza banja lathu. Choncho ndinayamba kuphunzira ndi a Mboni za Yehova. Koma mkazi wanga ankadana nawo kwambiri. Tsiku lina nditapita kumisonkhano ya Mboni za Yehova, anandiuza kuti ngati ndikufuna banja ndisiye kuphunzira. Ndinasowa chochita moti ndinasiyadi kuphunzira komanso kucheza ndi a Mboni. Komabe patapita nthawi ndinadzimvera chisoni chifukwa cholephera kutsatira zinthu zomwe zikanandithandiza. Tsiku lina ndili kuntchito anzanga anandionetsa zithunzi zolaula. Nditangoziona zinandisangalatsa komabe nthawi yomweyo zinandinyansa ndipo ndinayamba kudziimba mlandu kwambiri. Ndinakumbukira zimene ndinaphunzira m’Baibulo ndipo ndinkadziwa kuti Mulungu akhoza kundilanga. Koma nditayamba kuzionera mobwerezabwereza, ndinaona kuti zinalibe vuto lililonse moti chinangokhala chizolowezi. Ndinachita zimenezi kwa zaka 20 ndipo ndinkanyalanyaza mfundo zabwino zimene amayi anandiphunzitsa, kenako ndinaziiwali- ratu. Khalidwe langa linaipa chifukwa choonera zolaula. Ndinali wowola mkamwa ndiponso ndinkakonda nthabwala zotukwana. Ndinkaona kuti palibe vuto kugonana ndi wina aliyense moti ndinkagonananso ndi akazi ena. Tsiku lina nditadziyang’ana pagalasi ndinadzimvera chisoni ndiponso ndinadziona kuti ndine wachabechabe. Banja langa linatha ndipo moyo wanga unangokhala ngati nsanza zokhazokha. Ndiyeno ndinapemphera kwa Yehova mochokera pansi pamtima. Kenako ndinayambiranso kuphunzira Baibulo ngakhale kuti panali patadutsa zaka 20. Pa nthawiyi n’kuti bambo anga atamwalira ndipo mayi anga anali atabatizidwa. MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA: Zomwe ndinkachita zinali zosemphana kwambiri ndi mfundo zapamwamba za m’Baibulo. Pa nthawiyi ndinkafunitsitsa kukhala ndi mtendere wa m’maganizo womwe Baibulo limanena. Choncho ndinaganiza zosintha mmene ndinkayankhulira komanso khalidwe lokwiya msanga. Ndinaganizanso zosiya kuchita zachiwerewere, kutchova njuga, kumwa mwauchidakwa komanso kubera abwana anga. Anzanga akuntchito sankamvetsa chifukwa chimene ndinkafunira kusiya makhalidwe oipawa. Ndipo kwa zaka zitatu anayesetsa kuchita zinthu zofuna kundigwetsa ulesi. Nthawi zina akandimva ndikuyankhulanso mawu owola kapenanso ndikakwiya, ankasangalala ndipo ankanena kuti: “Eya! Ameneyo nde Joe timamudziwa ife.” Kunena zoona mawu amenewa ankandilasa mumtima. Ndipo ndinkaona kuti ndine wolephera basi. Kuntchito kwathu kunkapezeka mabuku ndiponso mavidiyo ambiri a zithunzi zolaula. Ndipo anzanga ankakonda kutumizirana zithunzizi pamakompyuta monga mmene ndinkachitira poyamba. Ndinkafunitsitsa nditasiya kuonera zolaula koma nthawi zonse anzangawo ankandikakamiza kuti ndizionerabe. Ndiyeno ndinafotokozera munthu yemwe ankandiphunzitsa Baibulo kuti andithandize. Iye anandimvetsera moleza mtima n’kundiwerengera mavesi a m’Baibulo omwe anandithandiza kudziwa mmene ndingathetsere vutolo. Anandilimbikitsanso kuti ndisasiye kupemphera kwa Yehova.—Salimo 119:37. Tsiku lina ndinaitanitsa anthu onse omwe ndinkagwira nawo ntchito. Kenako ndinawauza kuti atenge mowa n’kupatsa anzathu ena awiri amene anasiya uchidadwa. Komano chodabwitsa n’choti aliyense anadzuma n’kunena kuti: “Sitingachite zimenezo! Iwe sukudziwa kuti anthuwa akhala akuvutika ndi uchidakwa?” Ndiye nanenso ndinawayankha kuti: “Eetu, inenso ndikulimbana ndi vuto loonera zolaula.” Pompo anasiyiratu kundikakamiza. Patapita nthawi Yehova anandithandiza kusiyiratu khalidwe loipali. Mu 1999, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova ndipo ndimasangalala kwambiri kuti Yehova wandipatsanso mwayi wokhala ndi moyo wosangalala. Panopa ndimamvetsa chifukwa chake Yehova amadana ndi khalidwe loonera zolaula lomwe ndinkalikonda. Iye ndi Atate wachikondi ndipo ankafuna kunditeteza kuti ndisakumane ndi mavuto omwe anthu amene akhalidweli amakumana nawo. Ndaona kuti mfundo ya palemba la Miyambo 3:5, 6 ndi yoona. Lembali limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.” Choncho mfundo za m’Baibulo zanditeteza kwambiri komanso zandithandiza kuti zinthu zizindiyendera bwino.—Salimo 1:1-3. PHINDU LIMENE NDAPEZA: Nthawi yomwe ndinkaonera zolaula, ndinkadziona kuti ndine wachabechabe. Koma panopa ndimaona kuti ndine munthu wofunika, wamakhalidwe abwino, ndili ndi mtendere wamumtima, komanso ndimadziwa kuti Yehova anandikhululukira ndiponso amandithandiza. M’chaka cha 2000, ndinakwatira mkazi wokongola dzina lake Karolin. Nayenso amakonda kwambiri Yehova ndipo timakhala mwamtendere. Timaona kuti ndi mwayi waukulu kukhala m’gulu la Akhristu amakhalidwe abwino komanso okondana, omwe ali padziko lonse. ˇ Na. 4, 2016 13 KODI MUNGAYEREKEZERE ZOMWE MUMAKHULUPIRIRA NDI ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA? K ODI ndinu Mkhristu? Ngati ndi choncho, dziwani kuti simuli nokha. Padziko lonse pali anthu oposa 2 biliyoni omwe amati amatsatira Khristu, ndipo izi zikusonyeza kuti pafupifupi munthu mmodzi pa atatu alionse, ndi Mkhristu. Masiku ano pali zipembedzo zambiri zachikhristu, koma zimasiyana pa nkhani ya zikhulupiriro. Choncho zimene mumakhulupirira zingasiyane ndi zomwe anthu ena omwe amati ndi Akhristu amakhulupirira. Kodi kukhulupirira zilizonse kuli ndi vuto? Inde, chifukwa Akhristu amayenera kutsatira mfundo zopezeka m’Baibulo. 1 Anthu omwe ankatsatira Yesu Khristu anayamba kudziwika kuti “Akhristu.” (Machitidwe 11:26) Iwo sankadziwika ndi maina ena chifukwa panali chikhulupiriro chimodzi chokha chachikhristu. Popeza kuti Yesu Khristu ndi yemwe anayambitsa Chikhristu, Akhristu onse ankatsatira malangizo komanso zimene iye ankawaphunzitsa. Kodi zimene amaphunzitsa kutchalitchi kwanu zimagwirizana ndi zimene Khristu ankaphunzitsa, komanso zomwe otsatira ake oyambirira ankakhulupirira? Kodi mungadziwe bwanji ngati zimagwirizana? Njira yabwino kwambiri n’kudziwa zimene Baibulo limanena. FUNSO: Kodi Mulungu ndi ndani? ZIMENE BAIBULO LIMANENA: YANKHO: Ndi Yehova amenenso ndi Atate ake a Yesu, alibe mapeto komanso ndi Mulungu yemwe analenga zinthu zonse. ˙ “Nthawi zonse tikamakupemphererani, timayamika Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.”—Akolose 1:3. ˙ “Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse.”—Chivumbulutso 4:11. ˙ Onaninso Aroma 10:13; 1 Timoteyo 1:17. 2 3 FUNSO: Kodi Yesu Khristu ndi ndani? YANKHO: Ndi Mwana woyamba wa ZIMENE BAIBULO LIMANENA: Mulungu. Yesu anachita kulengedwa, choncho tingati ali ndi chiyambi. Ndipo amamvera mokhulupirika zimene Mulungu akufuna. ˙ “[Yesu] ndiye chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo, woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.”—Akolose 1:15. ˙ Onaninso Mateyu 26:39; 1 Akorinto 15:28. FUNSO: Kodi mzimu woyera n’chiyani? ZIMENE BAIBULO LIMANENA: YANKHO: Mzimu woyera ndi mphamvu ˙ “Tsopano Elizabeti atamva moni wa Mariya, khanda limene linali m’mimba mwakemo linadumpha. Ndipo Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyera.”—Luka 1:41. yomwe Mulungu amagwiritsa ntchito kuti akwaniritse zomwe akufuna. Koma si munthu. Anthu akhoza kudzozedwa ndi mzimu woyera komanso kupatsidwa mphamvu. 14 ˙ “Atate ndi wamkulu kuposa ine.”—Yohane 14:28. NSANJA YA OLONDA ˙ “Koma mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu.”—Machitidwe 1:8. ˙ Onaninso Genesis 1:2; Machitidwe 2:1-4; 10:38. Taganizirani izi: Yesu Khristu ankalemekeza kwambiri Malemba chifukwa ndi Mawu a Mulungu. Iye ankadana ndi anthu omwe ankalimbikitsa miyambo ya anthu m’malo mophunzitsa mfundo za m’Baibulo. (Maliko 7:9-13) Choncho tinganene kuti otsatira enieni a Yesu amayenera kutenga zikhulupiriro zawo m’Baibulo. Ndiyetu Mkhristu aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi zimene amaphunzitsa kutchalitchi kwathu zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena?’ Kuti muyankhe funsoli, mungachite bwino kuyerekezera zimene mumaphunzira ku tchalitchi kwanuko ndi zimene Baibulo limanena. Yesu ananena kuti tiyenera kulambira Mulungu m’choonadi ndipo choonadi chimenechi chimapezeka m’Baibulo. (Yohane 4:24; 17:17) Nayenso mtumwi Paulo ananena kuti tidzapulumuka ngati timadziwa “choonadi molondola.” (1 Timoteyo 2:4) Choncho zimene timakhulupirira ziyenera kugwirizana ndi mfundo zolondola za m’Baibulo. Zimenezitu n’zofunika kwambiri chifukwa kupanda kutero sitingadzapulumuke. 4 n’chiyani?Kodi Ufumu wa Mulungu FUNSO: YANKHO: Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba. Mfumu yake ndi Yesu. Posachedwapa Ufumuwu ukwaniritsa cholinga cha Mulungu padziko lonse. anthu onse abwino kumwamba? 5 amapitaKodi Ayi. Mulungu anasankha KODI ZIMENE TIMAKHULUPIRIRA TINGAZIYEREKEZERE BWANJI NDI BAIBULO? Tikukupemphani kuti muwerenge mafunso 6 amene ali m’nkhaniyi komanso muone mmene Baibulo likuyankhira mafunsowo. Muwerenge mavesi amene aikidwawo ndipo muone ngati akugwirizana ndi mayankho amene ali pansi pa mafunsowo. Kenako mudzifunse kuti, ‘Kodi zimene ndimaphunzira kutchalitchi kwathu zikugwirizana ndi zimene Baibulo likunenazi?’ Mafunso komanso mayankho omwe ali m’nkhaniyi akuthandizani kwambiri. Kodi mukufuna kuyerekezera zinanso zimene mumaphunzira kutchalitchi kwanu ndi zomwe Baibulo limanena? A Mboni za Yehova akhoza kukuthandizani kuti mudziwe mfundo zolondola za m’Baibulo. Mungachite bwino kupempha wa Mboni za Yehova kuti aziphunzira nanu Baibulo kwaulere. Mukhozanso kupita pawebusaiti yathu ya jw.org/ny. ˇ ZIMENE BAIBULO LIMANENA: ˙ “Mngelo wa 7 analiza lipenga lake. Ndipo kumwamba kunamveka mawu osiyanasiyana, akunena mokweza kuti: ‘Ufumu wa dziko wakhala ufumu wa Ambuye wathu ndi wa Khristu wake. Iye adzalamulira monga mfumu kwamuyaya.’ ”—Chivumbulutso 11:15. ˙ Onaninso Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10. FUNSO: ZIMENE BAIBULO LIMANENA: YANKHO: ˙ “Musaope, kagulu ka nkhosa inu, chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani Ufumu.”—Luka 12:32. anthu ochepa otchedwa “kagulu ka nkhosa” kuti akakhale kumwamba. Iwo akakhala mafumu limodzi ndi Yesu ndipo adzalamulira anthu padziko lonse. cholinga cha Mulungu 6 chokhudzaKodianthu komanso dziko FUNSO: lapansili n’chotani? YANKHO: Mu Ufumu wa Mulungu, dziko lapansili lidzakhala paradaiso ndipo anthu okhulupirika adzakhala ndi moyo wathanzi, mtendere wochuluka ndipo sadzafanso. ˙ “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye.”—Chivumbulutso 20:6. ˙ Onaninso Chivumbulutso 14:1, 3. ZIMENE BAIBULO LIMANENA: ˙ “Anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11. ˙ “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4. ˙ Onaninso Salimo 37:29; 2 Petulo 3:13. KODI BAIBULO LIMANENA ZOTANI? Kodi anthu ndi amene anayambitsa kupembedza? Kodi munthu ayenera kukhala m’chipembedzo chinachake? ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti anthu anaya- KODI MUNGAYANKHE BWANJI? mbitsa okha zoti azipembedza. Ena amakhulupirira kuti Mulungu amagwiritsa ntchito chipembedzo pofuna kuthandiza anthu kuti akhale naye pa ubwenzi. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? ˙ Inde “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi.” (Aheberi 10:24, 25) Choncho Mulungu amafuna kuti anthu amene amamulambira azisonkhana pamodzi mogwirizana. Pali “kupembedza koyera ndi kosaipitsidwa kwa Mulungu ndi Atate wathu.” (Yakobo 1:27) Mfundoyi ikusonyeza kuti pali chipembedzo choona chimene Mulungu anayambitsa. MFUNDO ZINANSO ZOMWE BAIBULO LIMANENA ˙ Anthu omwe amalambira Mulungu mogwirizana amayenera kukhulupirira mfundo zofanana. —1 Akorinto 1:10, 11. MFUNDO ZINANSO ZOMWE BAIBULO LIMANENA ˙ Mulungu amasangalala ndi chipembedzo chimene chimaphunzitsa mfundo za m’Baibulo.—Yohane 4: 23, 24. ˙ Zipembedzo zimene zimaphunzitsa mfundo za anthu n’zosathandiza.—Maliko 7:7, 8. ˙ Anthu a m’chipembedzo chimene Mulungu amavomereza ndi ogwirizana padziko lonse.—1 Petulo 2:17. CHINENERO Nditumizireni buku lakuti, Zimene Baibulo Limaphunzitsa? DZINA Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 15 m’buku ili, lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova Bukuli likupezekanso pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny ˙ Mwina ZIMENE BAIBULO LIMANENA ZIMENE BAIBULO LIMANENA Zimene Baibulo Limaphunzitsa ˙ Ayi ADIRESI s n o Mungapange dawunilodi magaziniyi ndi enanso a m’mbuyomu kwaulere p Baibulo likupezeka pa Intaneti m’zinenero zoposa 130 Pangani sikani kachidindo aka kapena pitani pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny wp16.4-CN 160322 Kuti mupeze adiresi yoyenera, onani tsamba 2
Similar documents
tiyeni atsikana!
• Ngati atsikana atadziwa kuti palibe kusiyana pakati pa mwamuna ndi mkazi, angathe kuchitapo kanthu pa mavuto awo; monga kukhala ndi mwayi wa maphunziro ndi maluntha opezera ndalama. • Angathens...
More informationGawoli mwachidule
achinyamata: Buku lophunzitsira – bukuli limathandiza makolo, opereka chithandizo, ndi achikulire onse omwe ali okhudzidwa kuti athe kuyankhulana ndi achinyamata. Cholinga cha pulogalamuyi ndi kuli...
More informationvolume 17400 - Tony Alamo Christian Ministries
chidwi paza AMBUYE mwakuti kupha- angelo aumdyerekezi. Elisa anawonetsa yonse yadziko lapansi idzagwidwa ndi tikiza azichimwene khumi sangafanane wantchito wake izi pamene asilikali aku chisoni, nd...
More informationBible Basics: Chichewa edition
“….muzisunga malembo ake ndi malamulo ake….kuti masiku anu achuluke.” Choncho, cholinga cha maphunziro ano mu buku lino, ndi kufuna kuphunzitsana zamb iri za malamulo amene‟wa ndi m‟mene t ingawasu...
More information